Genesis 44:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Ndipo ife tidaakuyankhani kuti, ‘Tili naye bambo wathu wokalamba ndi mbale wathu wina wamng'ono amene adabadwa bambo wathuyo atakalamba kale. Mkulu wake wa mnyamata ameneyo adamwalira kale. Choncho m'mimba mwa mai wake, yekhayu ndiye amene ali moyo, ndipo bambo wake amamkonda kwabasi.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’ Onani mutuwo |