Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:27 - Buku Lopatulika

27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 “Benjamini ali ngati mmbulu wolusa umene m'maŵa umapha ndi kudya zimene udagwira, ndipo madzulo umagaŵa zimene udagwirazo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 “Benjamini ali ngati mʼmbulu wolusa; umene mmawa umapha ndi kudya zofunkha, ndipo madzulo umagawa zofunkhazo,”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:27
25 Mawu Ofanana  

Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.


Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi.


Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, kufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pamutu wa Yosefe, ndi pakati pamutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake.


Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.


Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.


Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.


A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa.


Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.


Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,


Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.


wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;


Pamenepo ana a Benjamini anatuluka mu Gibea, naononga a Israele tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi.


Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m'mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa