Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:26 - Buku Lopatulika

26 Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, kufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pamutu wa Yosefe, ndi pakati pamutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, aufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Madalitso a bambo wako ndi amphamvu kupambana madalitso a mapiri amuyaya, kupambananso zabwino za ku zitunda zamuyaya. Zimenezi zidzakhala pamutu pa Yosefe, pamphumi pa kalonga amene adampatula pakati pa abale ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Madalitso a kholo lako ndi amphamvu kuposa madalitso a mapiri akale oposa zabwino za ku zitunda zamgonagona. Zonse izi zikhale pamutu pa Yosefe, pa mphumi pa wopatulika uja amene anapatulidwa pakati pa abale ake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:26
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito.


Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake.


Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.


Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.


Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa