Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.
Numeri 1:24 - Buku Lopatulika A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwa zidzukulu za Gadi adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. |
Ndi ana aamuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli.
Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'mizinda mwake?
owerengedwa ao a fuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.
owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.
Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;