Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la Manase, ndiwo adaoloka poyamba, ali okonzekera nkhondo, monga momwe Mose adaŵauzira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:12
9 Mawu Ofanana  

Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.


A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala mizinda ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.


Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele.


Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; ndipo anadza ndi mafumu a anthu, anachita chilungamo cha Yehova, ndi maweruzo ake ndi Israele.


Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza;


Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.


ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa