Yeremiya 49:1 - Buku Lopatulika1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'mizinda mwake? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana amuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'midzi mwake? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Za Aamoni, Chauta akufunsa kuti, “Kodi Israele alibe ana aamuna? Kodi alibe mloŵachuma? Chifukwa chiyani tsono anthu opembedza Milikomu alanda dziko la Gadi, ndipo akukhala m'mizinda yake? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova ananena izi: Amoni, “Kodi Israeli alibe ana aamuna? Kapena alibe mlowamʼmalo? Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi? Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi? Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.