Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 1:19 - Buku Lopatulika

Monga Yehova analamula Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Umu ndi m'mene adaŵerengera anthuwo m'chipululu cha Sinai.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:

Onani mutuwo



Numeri 1:19
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m'dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.


Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi.


Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.


Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.


Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.


Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.