Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 3:51 - Buku Lopatulika

51 Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 Ndipo Mose adapereka ndalama zoombolerazo kwa Aroni ndi kwa ana ake, potsata mau amene Chauta adalamula Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 3:51
11 Mawu Ofanana  

Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.


Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho mu Horebu chikhale cha Israele yense, ndicho malemba ndi maweruzo.


Monga Yehova analamula Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.


Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalande bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.


nupereke ndalama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna.


analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.


Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.


Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa