Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 1:6 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wampesa; ndipo ndidzataya miyala yake m'chigwa, ndi kufukula maziko ake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yake m'chigwa, ndi kufukula maziko ake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Chauta akuti, “Samariyayo ndidzamsandutsa bwinja, malo olimamo munda wamphesa. Miyala yake ndidzaitaya ku zigwa, ndipo maziko ake ndidzaŵafukula.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja, malo odzalamo mphesa. Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa ndipo ndidzafukula maziko ake.

Onani mutuwo



Mika 1:6
19 Mawu Ofanana  

Ndiponso ngati walowa kumzinda wina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumzindako, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko.


Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya.


Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.


Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula mizinda yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.


Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mzinda, ndimo udzangokhala muunda wopasulidwa.


Ndipo linga la pamsanje la machemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale pafumbi.


Chifukwa Inu mwasandutsa mzinda muunda; mzinda walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mzinda; sudzamangidwa konse.


Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.


Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse.


M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mzinda, ndi zonse zili m'menemo.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.