Yeremiya 51:25 - Buku Lopatulika25 Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 “Ndikukuimba mlandu, iwe phiri loononga, iwe amene umasakaza dziko lonse lapansi. Ndidzasamula dzanja langa pofuna kukulanga, ndi kukugubuduzira kunsi kuchokera pa mathanthwe ako. Ndidzakusandutsa phiri lopserera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 “Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga, amene umawononga dziko lonse lapansi,” akutero Yehova. “Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga, kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako, ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.