ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Mateyu 9:1 - Buku Lopatulika Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumzinda kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaloŵa m'chombo naoloka nyanja, nkukafika ku mzinda wakwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo. |
ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina.
Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.
Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera.
Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.
Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.