pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.
Mateyu 3:11 - Buku Lopatulika Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto. |
pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.
Pakuti ndidzathira madzi padziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;
Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.
Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.
Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.
pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.
Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?
Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye.
Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.