Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 3:16 - Buku Lopatulika

16 Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono Yohane ankaŵauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




Luka 3:16
24 Mawu Ofanana  

Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziwitsani mau anga.


kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.


pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa,


ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake.


Ndipo sindinamdziwe Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.


Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake.


pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.


Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.


Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.


Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa