Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Ndipo pamene ankapita mumseumo, adafika pena pamene panali madzi. Nduna ija idati, “Madzi si aŵa. Monga pali choletsa kuti ndisabatizidwe?” [

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:36
9 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:


nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao.


Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?


Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa