Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.
Mateyu 27:8 - Buku Lopatulika Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake mpaka lero mundawo umatchedwa “Munda wa Magazi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino. |
Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.
Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.
ndipo chinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanatchedwa Akeledama, ndiko, kadziko ka mwazi.)
Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.
Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.
Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mzinda, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.