2 Mbiri 5:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika kopambana patsogolo pa malo opatulika am'kati mwenimweni. Koma kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika, koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino. Onani mutuwo |