Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:9 - Buku Lopatulika

9 Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti, Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake, amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti, Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake, amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero zidapherezera zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Adatenga ndalama zija makumi atatu, mtengo wake umene Aisraele adaagamula,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:9
7 Mawu Ofanana  

Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.


Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;


Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti,


Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti,


nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa