Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.
Mateyu 26:7 - Buku Lopatulika anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo. |
Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.
Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.
Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.
Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.
Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda.
Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.
Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.