Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 10:1 - Buku Lopatulika

1 Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ntchentche zakufa zimaika fungo loipa m'mafuta onunkhira bwino. Choncho kupusa kwapang'ono kumatha kuwononga nzeru ndi ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira, choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:1
11 Mawu Ofanana  

Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.


Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.


Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja; chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.


ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osakanizika monga mwa machitidwe a wosakaniza; akhale mafuta odzoza opatulika.


Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri.


Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai.


Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa