Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
Mateyu 26:34 - Buku Lopatulika Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti usiku womwe uno, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha nati, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.” |
Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse.
Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.
Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.
Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.
Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.
Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.