Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 14:72 - Buku Lopatulika

72 Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

72 Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

72 Nthaŵi yomweyo tambala adalira kachiŵiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire kaŵiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 14:72
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.


Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.


Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.


Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.


Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira.


Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.


Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira.


Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa