Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:61 - Buku Lopatulika

61 Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

61 Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

61 Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, “Lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:61
19 Mawu Ofanana  

Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.


Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.


Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga?


Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri;


Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine.


Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira.


Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?


Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.


Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.


Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja;


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa