Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.
Mateyu 26:12 - Buku Lopatulika Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu wathira mafuta ameneŵa pa thupi langa kuti alidzozeretu lisanaikidwe m'manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. |
Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.
Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.
Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.
Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.