Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 16:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu.

Onani mutuwo Koperani




Marko 16:1
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.


Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.


Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.


Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.


Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;


Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata,


Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.


Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa.


Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.


Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira.


Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.


Koma tsiku loyamba la sabata, mbandakucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza.


Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa