Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
Mateyu 24:4 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Onetsetsani kuti wina asakunyengeni. |
Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.
Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.