Mateyu 2:18 - Buku Lopatulika Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau anamveka m'Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mau akumveka ku Rama, kulira ndi kubuma kwambiri: Rakele akulira ana ake. Akukana kumtonthoza, chifukwa ana ake asoŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kulira kukumveka ku Rama, kubuma ndi kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake; sakutonthozeka, chifukwa ana akewo palibe.” |
Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.
Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.
Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.
naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.
Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.
Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.