Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Mateyu 15:2 - Buku Lopatulika Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo? Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!” |
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Ndipo anyamata a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anati kwa Mordekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu?
Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?
Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?
ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: