Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Mateyu 12:2 - Buku Lopatulika Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.” |
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.
Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;
ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu.
Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenge chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye?
Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata?
Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?
Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.