Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.
Mateyu 10:34 - Buku Lopatulika Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzere kuponya mtendere, koma lupanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. |
Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.
Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.
chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale;