Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 6:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pamenepo kavalo wina, wofiira, adatulukira. Wokwerapo wake adaalandira mphamvu zothira nkhondo pa dziko lapansi, kuti anthu aziphana. Choncho adampatsa lupanga lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Pamenepo kavalo wina wofiira anatulukira. Wokwerapo wake anapatsidwa mphamvu yochotsa mtendere pa dziko lapansi ndi kuchititsa anthu kuti aziphana wina ndi mnzake. Iyeyu anapatsidwa lupanga lalikulu.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 6:4
17 Mawu Ofanana  

Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.


Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda;


Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzere kuponya mtendere, koma lupanga.


Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Ndipo chinaoneka chizindikiro china m'mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri.


Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.


Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.


Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa