Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 14:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo khamu la mzindawo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma anthu amumzindamo adagaŵikana, ena anali mbali ya Ayuda, ena anali mbali ya atumwi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Anthu a mu mzindamo anagawikana; ena anali mbali ya Ayuda, ena mbali ya atumwi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 14:4
18 Mawu Ofanana  

Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake.


Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;


Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo chifukwa cha Iye.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.


Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu,


Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mzinda; namuyesa kuti wafa.


Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu.


Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala,


Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano.


Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere.


Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?


Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa