Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 15:10 - Buku Lopatulika

10 Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Inu mai wanga, tsoka kwa ine kuti mudandibala ine munthu wokangana ndi wotsutsana ndi anthu pa dziko lonse. Sindidakongole kanthu kwa munthu kapena kukongoza munthu kanthu. Komabe anthu onse akunditukwana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine, munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse! Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu, komatu aliyense akunditemberera.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:10
32 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.


Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.


Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.


Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamuwerengera phindu.


Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.


Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.


Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.


Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera.


Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani.


Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.


koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;


Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;


Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.


Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa