Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 83:7 - Buku Lopatulika

Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Tiro.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Agebala ndi Aamoni ndi Aamaleke, Afilisti pamodzi ndi nzika za ku Tiro.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.

Onani mutuwo



Masalimo 83:7
7 Mawu Ofanana  

Ndipo masiku a Saulo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Giliyadi.


nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro.


Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;


ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum'mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati;


Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.


Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.