Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 15:2 - Buku Lopatulika

2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Ndidzalanga Aamaleke chifukwa cha kumenyana ndi Aisraele pa njira, pamene Aisraelewo ankachokera ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 15:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau.


Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.


ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.


Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.


Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?


Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa