Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Masalimo 83:1 - Buku Lopatulika Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, musakhalenso chete. Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu. |
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.
Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.