Masalimo 82:7 - Buku Lopatulika Komatu mudzafa monga anthu, ndipo mudzagwa monga wina wa akulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komatu mudzafa monga anthu, ndipo mudzagwa monga wina wa akulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe mudzafa ngati anthu onse, ndipo mudzagwa ngati kalonga wina aliyense.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.” |
Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe.
kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.