muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka, ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!
Masalimo 81:16 - Buku Lopatulika Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikadakudyetsani ndi ufa wosalala watirigu, ndipo ndikadakukhutitsani ndi uchi wam'thanthwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.” |
muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka, ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona!
Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.
Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
Ndipo amuna a pamzinda anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa, Chozuna choposa uchi nchiyani; ndi champhamvu choposa mkango nchiyani? Pamenepo ananena nao, Mukadapanda kulima ndi ng'ombe yanga, simukadatha kumasulira mwambi wanga.