Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Masalimo 148:1 - Buku Lopatulika Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga. |
Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.
Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!