Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 89:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu, Inu Chauta, zimatamanda kukhulupirika kwanu mu msonkhano wa oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova, kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 89:5
24 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.


Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi? Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo?


Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.


Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.


Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.


Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.


Ana ake akataya chilamulo changa, osayenda m'maweruzo anga,


Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse, ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Kumwamba kulalikira chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.


Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.


kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.


ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa