Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
Masalimo 140:8 - Buku Lopatulika Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, musampatse munthu woipa zokhumba zake. Musathandizire chiwembu chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova; musalole kuti zokonza zawo zitheke, mwina iwo adzayamba kunyada. Sela |
Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.
Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.
Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa.
Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.