Masalimo 118:10 - Buku Lopatulika Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adani a mitundu yonse adandizinga, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a mitundu yonse anandizinga, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga. |
Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.
Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo.