Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.
Masalimo 103:2 - Buku Lopatulika Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse. |
Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.
Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonyika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa.
Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.
Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?
pamenepo mudzichenjera mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.
Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri mu Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.
Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a mu Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova.