Masalimo 1:4 - Buku Lopatulika Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu oipa sali choncho, ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sizitero ndi anthu oyipa! Iwo ali ngati mungu umene umawuluzidwa ndi mphepo. |
Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.
Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.
Koma khamu la achilendo ako lidzafanana ndi fumbi losalala, ndi khamu la oopsa lidzakhala monga mungu wochokachoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.
Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.