Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 13:3 - Buku Lopatulika

3 Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Nchifukwa chake adzazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, kapena mame okamuka msanga. Adzamwazika ngati mungu wouluzika kuchokera pa malo opunthira tirigu, kapena ngati utsi wotuluka pa zenera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa, ngati mame amene amakamuka msanga, ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu, ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:3
11 Mawu Ofanana  

Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?


Anditembenuzira zondiopsa, auluza ulemu wanga ngati mphepo; ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo.


Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.


Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.


Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.


Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, ndipo zinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.


Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.


lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.


Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa