Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 13:24 - Buku Lopatulika

24 Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Chifukwa cha kuipa kwanuko, ndidzakumwazani ngati mankhusu, onka nauluka ndi mphepo yakuchipululu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:24
19 Mawu Ofanana  

Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.


Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.


Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.


Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la Tsoka lao.


Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwe; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.


Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga; waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga, Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Yuda, monga mopondera mphesa.


Ndipo othawa ake onse m'magulu ake onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa kumphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko.


Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Ndinati, Ndikadawauzira ndithu, ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa