Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 7:2 - Buku Lopatulika

ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwo adaaona kuti ophunzira ake ena ankangodya chakudya osasamba m'manja moyenera (ndiye kuti mosasamala mwambo wosamba m'manja.)

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba.

Onani mutuwo



Marko 7:2
12 Mawu Ofanana  

Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya.


Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?


Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.


ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;


Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.


Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.


ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.