Marko 4:9 - Buku Lopatulika Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adati, “Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.” |
Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.