Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:11 - Buku Lopatulika

11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, siidzamkhudza imfa yachiŵiri.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:11
16 Mawu Ofanana  

Amene ali ndi makutu akumva, amve.


Amene ali ndi makutu, amve.


Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.


Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.


Ngati wina ali nalo khutu, amve.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.


Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.


Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa