Marko 2:7 - Buku Lopatulika Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kodi Iyeyu angalankhule bwanji motere? Si kunyoza Mulungu kumeneku? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?” |
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?
Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?
Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?
Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.
kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu?