Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Marko 1:7 - Buku Lopatulika Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula zingwe za nsapato zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kulalika kwake ankati, “Pambuyo panga pakubwera wina wamphamvu kuposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuŵerama nkumasula zingwe za nsapato zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. |
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi?
Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo.
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake.
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.
Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.